( Verse 1)
Delira mkazi wangawe
Wachitiranji zoterezi?
kundigulitsa manja mwa adani
Delira
Pondifunsa za chinsisi changa
ndikaona ngati ndichikondi
koma kunali kunditchera sapha
abale
Ndikanaziwa za mumtima mwako
Ndithudi mkazi ndikanakupewa
Koma za mumtima ndi za wekha
ndaona
Mmesa umati umandikonda
nanga chikondicho chimatero?
Kumuika nzako pamavuto ine ndalira
( Chorus)
Inu Musamale!
Musamale ndi anthu enawa
enawa!
zochita zawo ndi a Delira
tsiku lina adzakupelekani
Musamale
Inu Musamale
Musamale ndi anthu enawa
enawa!
zochita zawo ndi a a petulo
aPetulo!
tsiku lina adzakukani
Musamale
Inu Musamale
Musamale ndi anthu enawa
enawa!
zochita zawo ndi a Yudasi
aYudasi eeee
tsiku lina adzakugulitsani
Musamale
Inu Musamale!
Musamale ndi anthu enawa
enawa!
zochita zawo ndi a Delira
aDelira
tsiku lina adzakupelekani
Musamale
(Verse 2)
……………………………………….
Inu abale ngati mufuna bwenzi
kuli bwino kusakha akhale Yesu
iye ndi bwenzi losakumudwitsa ngati enewa
Amasamala amatetenza ,chikondi chake ndichapamtima sadzalolera kuti muvutike zoona.
Abwenzi apadziko amakukonda
pamene zinthu zako zili bwino,
pamavuto amakusiya wekha wekha
Musawaone kutsekelerako mumtima mwawo muli nkhondozo,
tsiku lina zidzaonekera iwe samala
(Back to the chorus)
Inu Musamale!
Musamale ndi anthu enawa
enawa!
zochita zawo ndi a Delira
tsiku lina adzakupelekani
Musamale
Inu Musamale
Musamale ndi anthu enawa
enawa!
zochita zawo ndi a a petulo
aPetulo!
tsiku lina adzakukani
Musamale
Inu Musamale
Musamale ndi anthu enawa
Enawa!
zochita zawo ndi a Yudasi
aYudasi eeee
tsiku lina adzakugulitsani
Musamale
Inu Musamale!
Musamale ndi anthu enawa
enawa!
zochita zawo ndi a Delira
aDelira
tsiku lina adzakupelekani
Musamale