Camillius Simakweri ndi mwana wachitatu kubadwa m’banja mwawo ndipo amakhala ku Mchinji Chipata Border.kumudzi kwawo ndi ku Chileka mu mzinda wa Blantyre koma anakhazikika ku Chilomoni.

Camillius anayamba kuyimba mu chaka cha 2014 pomwe amachita chidwi kuyambila ali ku primary amakonda kuyambitsa nyimbo mpaka kufikira pomwe anayamba kupeka nyimbo yekha.
Pakadali pano Camillius ali ndi chimbale chimodzi chotchedwa Nena Zoona chomwe anajambula ndi Mvahiwa Hakhe ndipo pakadali pano ali mkati mojambulanso chimbale china chomwe pakadali pano wajambulako nyimbo zokwana 6 ndi Princox ku Dynasty Studio.Kupatula kuyimba Camillius amapanga bussiness komanso ulimi.