Mphatso Haji Banda anabadwa pa 27 July, 1991 ndipo m’banja mwawo anabadwa ana asanu ndipo iye ndi omaliza kubadwa ndipo akukhalira ku Area 24 mu mzinda wa Lilongwe.

Mphatso anayamba kuyimba mu chaka cha 2009, “Kuyimba zinayambira ku maloto kenaka ndimati ndikakhala ndimazimva ngati wina wake akundiyimbira nyimbo ndikatero ndimatenga kope ndi cholembela kumayilemba nyimbo ija ndipo ndinadzaganiza zokalowa mu studio” adatero Mphatso.
Mphatso adatulutsako zimbale ziwiri ndipo chimbale choyamba mutu watu wake unali Yesu ndiye nyali ndipo chimbale chachiwiri mutu wake unali Pemphani ndipo chidzapatsidwa.
Pakadali pano mphatso watulutsako nyimbo zatsopano ziwiri monga Chikhulupiliro komanso Mukanena za ine yomwe yatuluka kumapeto a mwezi wa March.