Rose Mwalure anabadwa mu chaka cha 1985 ndipo ndi mwana oyamba kubadwa m’banja lawo la ana anayi.Kumudzi kwawo ndi kwa Khayano T/A Nthilamanja boma la Mulanje.Kuyimba payekha anayamba mu chaka cha 2017 ndipo ali ndi chimbale chimodzi chomwe anachitulutsa mu 2021 pa 3 April ndipo pakadali pano akujambula chimbale chachiwiri chomwe sadachimalizitse.Chimbale chake choyamba chimatchedwa Ndili ndi Mantha ndipo chachiwiri chimatchedwa Mundiyankhe.Pakadali pano Rose akukhalira ku Capetown m’dziko la South Africa.
