Home » MABVUTO PANGANANI – BIOGRAPHY

MABVUTO PANGANANI – BIOGRAPHY

by Malawi Gospel Music
470 views

Mabvuto Panganani anabadwa mu Chaka cha 1982 mu banja la ana 4 mwa ana atatu ndi akazi wamamuna alipo yekha komanso wotsiliza pobadwa woyamba kubadwa ndi Teleza kenako Tikalipo ndikubwera Solobina ndipo mwa Chisomo cha Mulungu onse akadalipo ndipo ali m’mabanja.Makolo omwe anabala Mabvuto ndi ochokera ku mtundu wa chichewa bambo Panganani ku chokera ku Lilongwe ndi a Tombi from Dowa koma mwa chifuniro cha Mulungu onse Makolo anatsikira kuli chete.

Dzina loti Mabvuto linapelekedwa ndi bambo ake a Panganani chifukwa ndi nthawi yomwe mayi ake anasiya dziko lapansi mu njira ya imfa koma nkuti panthawiyi ali ndi miyezi yochepa chibadwire choncho bambo ake anaganiza zomupatsa dzinali.

Ana onse anakula movutika kwambiri chifukwa anakakhala ndi agogo aku chikazi omwe ankadziwika ndi dzina loti WATCHI pa nthawi yi nkuti atangochoka ku Zimbabwe banja litatha ndi amuna awo ku Zimbabwe ko choncho anali pa umasiye wa dzawoneni ku nkhoma amagonera mango ophika kapena chinangwa.Ali mkati mozunzika choncho bambo Panganani adamwaliranso cha ma 1992 zomwe chinalitu tsopano chipsyinjo pa moyo wawo makamaka iyeyo ngati wachichepele kenako anasamukira ku mudzi ku Dowa ndi agogo akazi aja kulondola achimwene awo komanso ngati ku mudzi komanso sanakhalitse nkumamwaliranso.

Wakusapo ziweto kwa zaka 13 za anthu koma moyo osasintha kumangokhalabe mu umphawi wadzawoneni .

Sukulu kunali kovuta kwambiri kuti aphunzire koma mwa Chisomo cha Mulungu ang’ono awo amai ake akazi a senior group a Mtsinje ndiwo anamuchotsa ku mudzi kubwelera ku Lilongwe ndi kupanga chothekera ku kumupititsa ku Sukulu. Ma Sukulu omwe waphunzirapo ndi Mbalame FP School, Dowa ,Tsabango FP School ndi M’chitanjiru FP School.Secondary anaphunzira ku M’chitanjiru Community day Secondary School komanso Mulodza community day Secondary School Ndipo fees amalipira ndi a SOS.

CHIPEMBEDZO

Mabvuto Panganani ndi mkristu wa Chikatolika yemwe amapemphera ku St Don Bosco Parish ndipo amadziwika ndi dzina loti Luka Panganani.Anakwatirana ndi Petronia( Hellena) ndipo ali ndi ana atatu Nicholas, Norris komanso Yohane.

Chiyambi cha mayimbidwe ake chinayambila mu choir koma kuyamba kuyimba pa yekha anayamba mu chaka cha 2017 ndi pomwe anayamba kulemba ndi kumajambula nyimbo ndipo wajambula ma studio angapo ndipo akanajambulabe.

Spread the love

You may also like

Leave a Comment

malawigospelmusic.com is a Christian music website with all Malawian gospel Music and any gospel News.malawigospelmusic.com offer services like song lyrics,Audio upload,poems,Music video upload on our You Tube channel called Malawian Gospel Music, Artist biography, Extended playlist (EP),Article, Album and Banner on website. For inquiry contact these numbers 0888 069 117/0885 572 836 or 0983 592 032/0994 56 15 46 or info@malawigospelmusic.com

All Rights Reserved – Designed and Developed by Kay Dee Media