Home » HERO K.ARTNESS – BIOGRAPHY

HERO K.ARTNESS – BIOGRAPHY

by Malawi Gospel Music
321 views

Artness Ngalauka kubadwila ku Dedza m’mudzi mwa a Mfutso,kukulila ku Lilongwe ku Chilinde.Artness anabadwa pa 29 September 1983, mwana oyamba kubadwa m’banja la ana 4,akazi okhaokha.

Maitanidwe amayimbidwe anamufikila ali ndi 8 yrs pomwe a malemu Shadreck Wame anakhala naye chidwi kwambili ku Kasungu pomwe anakaimba pa msonkhano wawo ndipo miyoyo yochuluka inatembenuka mtima chifukwa Cha maimbidwe ake.Artness ali ndi zaka 10 amkapangitsa anthu ambili kubwera ku msonkhano wa 5 days wa a Shadreck Wame ku Kasungu komwe amakhala pa nthawi imeneyo.

Kuimba kunapitilila ku kwaya yomwe amaimba mu seventh day Adventist Church kufikila pomwe Artness anakula.Chidwi choyamba kuimba ngati soul artist chinakhazikika mwa iye 2008 pomwe anaganiza zotulutsa chimbale choyamba chomwe ankati Tikalowako Bwanji ndipo nyimbozi zimkaseweredwa kwambili pa Zodiac ndi Joe Mwase koma zinazangozizila chifukwa chosapanga promote nyimbozo.

Mu 2015 Artness anatulutsa chimbale china chotchedwa Ndipitabe chomwe anajambula ndi producer Anthony Makuta ndipo anthu anachilandila kwambili ndipo anachipanga launch ku South Africa mu 2018.Mu 2020 anatulutsa chimbale china chotchedwa Alipo Ondimenyera chomwe anapanganso launch ku RSA komko.2022 anatulutsa chimbale china chotchedwa Ndapanga Chisankho chomwe sanapange launch koma nyimbo zili pa website.Pano Artness akuyembekezeka kutulutsa chimbale china chomwe mutu wake ndi WAMOYO chomwe chikhale chikukhazikitsidwa mkatikati mwa 2024.Artness ali ndi dzina koma lomwe amatchuka nalo ku maimbidwe ndi HERO K.

Spread the love

You may also like

Leave a Comment

malawigospelmusic.com is a Christian music website with all Malawian gospel Music and any gospel News.malawigospelmusic.com offer services like song lyrics,Audio upload,poems,Music video upload on our You Tube channel called Malawian Gospel Music, Artist biography, Extended playlist (EP),Article, Album and Banner on website. For inquiry contact these numbers 0888 069 117/0885 572 836 or 0983 592 032/0994 56 15 46 or info@malawigospelmusic.com

All Rights Reserved – Designed and Developed by Kay Dee Media