(Hook)
Ooh Yesu wanga
(Ndibwenzi)
Ooh Yesu Wanga
(Eeeh ndibwenzi)
Ooh Yesu wanga
(Ndibwenzi)
Ndibwenzi Lokometsetsa..
Ooh Yesu wanga
(Ndibwenzi)
Ooh Yesu Wanga
(Eeeh ndibwenzi)
Ooh Yesu wanga
(Ndibwenzi)
Ndibwenzi lokondetsetsa..
(Verse)
Abwenzi Am’dziko timakhala nawo//
Kwanthawi yochepa ndikusiyana//
Dzuwa likalowa titsanzikana//
Mugone bwino tionana mawa//
Tikasiyana palibe amadziwa//
Chimene chimchitikila nzakeyo//
Pokhapokha alandile uthenga//
Nzako wadwala ‘pena wamwalira//
Koma ndili ndibwenzi langa lokonda//
Nthawi zonse samandisiya//
Kulikonse kumene ndingapite//
Akhala nane kundiyang’anira//
Samagona kapena kuodzera//
Amanditeteza usiku onse//
M’banda kucha andidzutsa ndimphamvu//
Masana, madzuro akhala nane//