Home » Lyrics » LOYCE YOTAMU MKWEHIWA FT EVANCE WATSOPANO MELEKA – MULUNGU ODABWITSA LYRICS

LOYCE YOTAMU MKWEHIWA FT EVANCE WATSOPANO MELEKA – MULUNGU ODABWITSA LYRICS

by Malawi Gospel Music
541 views

VERSE 1

Oposa ndani inu Yehova mwini chilengedwe chonse kumwamba ngakhale padziko
Inu ndinu Mulungu
Mulungu wazisomo okondaliese ngakhale osakudziwani Mulungu inu muwayang’anira
Inu ndinu Mulungu
Mumadyesa mbalame zosalima mudzisunga dzanja lanu Mulungu inu ndinu wachikondi
Inu ndinu Mulungu
Mudziwa zinsinsi za wina aliese ngakhale za pansi pa nyanja koma simukwiya mumatikonda ife.

CHORUS

Mulungu inu ndinu odabwitsa mulibe nsankho mumakonda wina aliese simuona nkhope ndaona dzanja lanu Yehova likumenya nkhondo pakanapanda inu Yesu bwenzi ndili chabe Ambuyeyesu bwelani mukhale mbari yanga poyesedwa ine dziko mudzikhala nane, Ambuyeyesu bwelani mukhale linga Langa poyesedwa ine dziko mudzikhala nane

VERSE 2 Evance

Mumachiza nthenda zosachizika palibe nthenda yomwe ingakulakeni Mulungu wazatheka bwanji inu
Inu ndinu Mulungu
Mukamadalisa simuona nkhope ochimwa muwapasa chuma mtendere tipeza Kwa inu
Inu ndinu Mulungu
Inu ndiye bwenzi la ochimwawo,akhungu ngakhale olema Mulungu opanda tsankho
Inu ndinu Mulungu
Ngakhale ndiende chigwa Cha nthunzi wa imfa Mbuye sindidzaopa poti inu ndinu moyo wanga

CHORUS

VERSE 3

Zomwe timapempha inu mumatipasa koma sitichedwa kukuiwalani chikondi chanu mumatipasabe
Inu ndinu Mulungu
Timakupembedzani Mbuye mwachinyengo kusangalasa dzikoli koma simumakwiya mutikonda ife
Inu ndinu Mulungu
Amasiye inu
mumawadyesa amisala ngakhale osowa Mbuye onsewa muwasunga ndinu
Inu ndinu Mulungu
Palibe wina Mbuye ofananu ndinu Mulungu wachikondi kufika lero ine ndi chisomo
Inu ndinu Mulungu

CHORUS

Mulungu inu ndinu odabwitsa mulibe tsankho mumakonda wina aliese simuona nkhope ndaona dzanja lanu Yehova likumenya nkhondo pakanapanda inu Yesu bwenzi ndili chabe Ambuyeyesu bwelani mukhale mbari yanga poyesedwa ine dziko mudzikhala nane Ambuyeyesu bwelani mukhale linga langa poyesedwa ine dziko mudzikhala nane….

malawigospelmusic.com is a Christian music website with all Malawian gospel Music and any gospel News.malawigospelmusic.com offer services like song lyrics,Audio upload,poems,Music video upload on our You Tube channel called Malawian Gospel Music, Artist biography, Extended playlist (EP),Article, Album and Banner on website. For inquiry contact these numbers 0888 069 117/0885 572 836 or 0983 592 032/0994 56 15 46 or info@malawigospelmusic.com

All Rights Reserved – Designed and Developed by Kay Dee Media